Luso La Joe Kellz Mpatali | The Nation Online

Joe Kellz

Kellz ndi katakwe ku nkhani ya maimbidwe. Mwachidule, tingoti Kellz amatha. Masiku apitawa iye adatulutsa nyimbo yokumbukira luso la katswiri wa maimbidwe m’dziko muno yemwe adatisiya, Wambali Mkandawire. Tikunena pano, nyimboyi ili ponseponse.  MARTHA CHIRAMBO adacheza naye motere:

Joe Kellz | The Nation Online
Joe Kellz: Ndinkayesera ena.

Tikudziweni?

Ndine Kelvin Jonathan Pangani koma ndimadziwika ngati Joe Kellz. Ndidabadwira komanso kukulira kwa Chinsapo 2, mumzinda wa Lilongwe. Pakadalipano ndimakhala ku Chigwirizano, mumzinda womwewo wa Lilongwe. Ndine woyamba kubadwa m’banja la ana awiri.

Kodi maphunziro mudafika nawo pati?

Sukulu yanga ya pulaimale ndidaimba m’sukulu zosiyanasiyana monga Maranatha ndipo kuchoka uko adandisankhira ku sekondale ya Madisi, m’boma la Dowa m’chaka cha 2009. Kuchokera ku Madisi adandisankhira ku sukulu ya ukachenjede ya Luanar ndipo ndidali ku Bunda College pomwe ndidabwerako ndi Bachelors Degree in Agricultural Development Communication, m’chaka cha  2018.

Nanga mumatani pamoyo wanu?

Ndine woimba. Ndimalemba, kupeka komanso kujambula nyimbo mwa zina. Ndimaphunzitsanso za maimbidwe kuphatikizapo piano. Ndagwirapo ntchipo ndi mabungwe ambiri  poimba nyimbo zokhudza ntchito zawo. Kupatula apo ndimachitanso bizinesi zing’onozing’ono.

Mudayamba bwanji luso lanuli?

Ndidayamba kuimba ndili wamng’ono kwambiri. Ndinkakonda kuyesezera anthu oimba ena ndikamvera nyimbo zawo. Ndimakhala ndichimwemwe kwambiri ndikamaimba ndikumazimvera ndekha mmene ndikuimbira. Kenako ndidaganiza zoyamba nawo kuimba makwaya akutchalitchi. Kumeneko ndi kumene kudasula luso langa.

Ndi mavuto otani omwe mumakumana nawo pa ntchito yanu?
Malawi ndi limodzi mwa maiko amene sitidayambe kulemekeza luso. Izi zimachitika chifukwa chiwerengero chambiri cha anthu m’dziko lathu ndi opereweredwa ndipo sangakwanitse kumapeza ndalama yogulira luso kapena yolipirira kuti akaonelere luso lathu. Chifukwa cha chimenechi oimba m’dziko lanthu sitikhala ndikuthekera kopeza makobidi kudzera m’ma luso athu.

Nanga mumathana nawo bwanji?

Ndizovuta kuti tithane ndivutoli chifukwa ndizoyenera kuyambira kumtunda kwa akuluakulu kubweretsa njira zoti anthu ambiri m’dziko lathu lino azikhala ndi makobili ochitira zisangalalo amene m’Chingerezi timati Luxury Money.
Izi sizingachitike tsiku limodzi kapena chaka chimodzi. Ndi ndondomeko yaitali kwambiri. Kotero ine ngati mmodzi mwa oimba ku Malawi ndine wothokoza kwa anthu ochepa omwe amakwanitsa kugula nyimbo zathu komanso kulipira ndalama zankhaninkhani kuti aonere luso lathu.
Kwa amene sangakwanitse kutero ndimathokozanso chifukwa cha mafuno abwino amene mumatipatsa mukamvera maluso athu.

N’chiyani chomwe mumafuna chitasintha kuti luso lanu lipite patsogolo?

Ku Malawi kulibeko kampani zopititsa patsogolo luso (Promotion companies).
Ndimaganiza kuti pa anthu amene ali ndikuthekera koika mpamba wawo mu maluso osiyanasiyana atati achita motero zitha kuthandiza kwambiri.
Ndanena izi chifukwa ndikudziwa kuti ku Malawi tili ndimaluso ambiri amene amakanika kubwera poyera chifukwa chosowa ndalama ndi zipangizo zina zowayenereza.

Mungamulimbikitse bwanji munthu amene akufuna kutsata mapazi anu?

Kwa onse amene amafuna atadzakhala oimba ndingowamema kuti akhale ndikena kamene angadalire kuti kaziwadyetsa tsiku ndi tsiku kenako n’kuyamba kuimba. Chifukwa luso loimba m’dziko lathu lino limatenga nthawi yaitali kuti liyambe kubweza zake. Ngati uli wachinyamata ndipo uli ndi kuthekera kochita maphunziro ako pitiriza ndithu osasiira panjira.

Kodi muli pa banja?

Sindili pa banja.

Mawu anu owonjezera ndi wotani?

Pomaliza ndingothokoza kwa onse amene amakonda kumvera nyimbo zanga.
Kumazipempha pa wailesi, kugula nyimbozi zikatuluka kumene, komanso kubwera kuzoimbaimba. Mulungu aziwadalitsa ndipo ine ndipitiriza kukubweretserani nyimbo.

Credit